Alimi a Ngombe za mkaka amafuna kuti ngombe zawo zizitulutsa mkaka ochuluka kuti apeze phindu, izi nayi fundo 7 zothandizila kachulukitsidwe ka mkaka kuti mupeze phindu lochulukilapo.
Ndizofunikira kwambiri kudyetsela chakudya chopeleka phamvu chokwanila ndipo chamulingo okwanila ,kudyetsela ma vitamini ndi michere yofunika ku ngombe , kuonetsetsa kuti pali chakudya ndi udzu wabwino nthawi zonse ,kukonzekela chakudya cha ngombe nthawi ya dzuwa ,kuonetsetsa kuti muli ndi madzi oyela bwino ndipo a ukhondo mu gome lomwela ngombe ndipo kusintha chakudya cha ngombe pangonopangono ndi cholinga choti musatsokoneze ka gayidwe ka chakudya cha ngombe .